Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Chitetezo cha Farao chidzakhala chochititsa manyazi kwa amuna inu,+ ndipo kubisala mumthunzi wa Iguputo kudzakhala chinthu chopereka chitonzo.+

  • Yesaya 31:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Koma Aiguputowo ndi anthu ochokera kufumbi.+ Si Mulungu ayi. Mahatchi awo ndi zinyama,+ osati mzimu. Yehova akadzatambasula dzanja lake, amene akupereka thandizo adzapunthwa, ndipo amene akuthandizidwawo adzagwa.+ Onsewo adzatha nthawi imodzi.

  • Yeremiya 17:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Yehova wanena kuti: “Wotembereredwa ndi munthu aliyense wokhulupirira mwa munthu aliyense wochokera kufumbi.+ Wotembereredwa ndi munthu amene amadalira mphamvu za dzanja la munthu,+ komanso amene mtima wake wapatuka kuchoka kwa Yehova.+

  • Maliro 4:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pamene tili ndi moyo, maso athu akulefuka chifukwa choyembekezera thandizo lomwe silikubwera.+

      Pofunafuna thandizo, tadalira mtundu wa anthu amene sangabweretse chipulumutso.+

  • Ezekieli 17:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Farao sadzamutumizira gulu lalikulu la asilikali ndi khamu la anthu kuti amuthandize pankhondo.+ Sadzamuthandiza mwa kumanga chiunda chomenyerapo nkhondo ndiponso mpanda womenyerapo nkhondo n’cholinga chakuti aphe anthu ambiri.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena