1 Mafumu 7:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Anaumba zipilala ziwiri zamkuwa.+ Kutalika kwa chipilala chilichonse kunali mikono 18, ndipo pankafunika chingwe chotalika mikono 12 kuti ayeze kuzungulira chipilala chilichonse.+ Yeremiya 52:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Ponena za zipilalazo, chipilala chilichonse chinali chotalika mikono* 18,+ ndipo chinali kuzunguliridwa ndi chingwe chotalika mikono 12.+ Chipilala chilichonse chinali champhako ndipo kuchindikala kwake kunali kofanana ndi mphipi ya zala zinayi.
15 Anaumba zipilala ziwiri zamkuwa.+ Kutalika kwa chipilala chilichonse kunali mikono 18, ndipo pankafunika chingwe chotalika mikono 12 kuti ayeze kuzungulira chipilala chilichonse.+
21 Ponena za zipilalazo, chipilala chilichonse chinali chotalika mikono* 18,+ ndipo chinali kuzunguliridwa ndi chingwe chotalika mikono 12.+ Chipilala chilichonse chinali champhako ndipo kuchindikala kwake kunali kofanana ndi mphipi ya zala zinayi.