Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mafumu 7:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ndiyeno Hiramu anaika zipilala+ zija pakhonde+ la kachisi. Chipilala chimodzi anachiika mbali ya kudzanja lamanja n’kuchitcha Yakini. Chipilala china anachiika mbali ya kumanzere n’kuchitcha Boazi.

  • 2 Mafumu 25:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Chipilala chilichonse kutalika kwake chinali mikono 18,+ ndipo mutu+ wake unali wamkuwa. Mutuwo kutalika kwake kunali mikono itatu, ndipo maukonde ndi makangaza*+ amene anazungulira mutuwo, onse anali amkuwa. Chipilala chachiwiri chinalinso ndi maukonde ofanana ndi amenewa.

  • 2 Mbiri 3:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Ndiyeno kumaso kwa nyumbayo anamangako zipilala ziwiri+ zazitali mikono 35. Mutu+ wa chipilala chilichonse umene unali pamwamba pake unali wautali mikono isanu.

  • Yeremiya 52:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ponena za zipilalazo, chipilala chilichonse chinali chotalika mikono* 18,+ ndipo chinali kuzunguliridwa ndi chingwe chotalika mikono 12.+ Chipilala chilichonse chinali champhako ndipo kuchindikala kwake kunali kofanana ndi mphipi ya zala zinayi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena