22 Mutu wa chipilala chilichonse unali wamkuwa.+ Mutuwo kutalika kwake kunali mikono isanu,+ ndipo maukonde ndi makangaza amene anazungulira mutuwo,+ onse anali amkuwa. Chipilala chachiwiri chinalinso ndi maukonde ofanana ndi amenewa komanso chinali ndi makangaza.+