3 Khonde+ la kutsogolo kwa chipinda chachikulu* cha nyumbayo linali mikono 20 m’litali, kufanana ndi m’lifupi mwa nyumbayo. Khondelo linali kutsogolo kwa nyumbayo, ndipo linali mikono 10 m’lifupi mwake.
12 Kuzungulira bwalo lalikulu panali khoma la miyala yosema lotalika mizere itatu+ kuchokera pansi, ndi mzere umodzi wa matabwa a mkungudza pamwamba pake. Bwalo lamkati+ la nyumba+ ya Yehova ndi khonde+ la nyumbayo, zinamangidwanso mofanana.
48 Kenako ananditengera pakhonde la nyumbayo.+ Pamenepo anayeza chipilala cham’mbali cha khondelo ndipo anapeza kuti chinali mikono isanu mbali iyi ndi mikono isanu mbali inayo. M’lifupi mwa khomo la nyumbayo munali mikono itatu mbali iyi ndi mikono itatu mbali inayo.