41 Tsopano m’mwezi wa 7, Isimaeli+ mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama,+ anapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa+ pamodzi ndi amuna ena 10.+ Isimaeli anali wa m’banja lachifumu+ ndipo analinso mmodzi mwa akuluakulu a mfumu. Atafika kumeneko anayamba kudya chakudya pamodzi.+