-
Yeremiya 41:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ndiyeno Yohanani+ mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a magulu ankhondo amene anali naye anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa. Anthu amenewa anawalanditsa m’manja mwa Isimaeli mwana wa Netaniya amene anawagwira atapha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu. Analanditsa amuna amphamvu, amuna ankhondo, akazi awo, ana ndi nduna za panyumba ya mfumu. Yohanani analanditsa anthu amenewa ku Gibeoni.
-