4 Ndiyeno anayenda kudutsa m’dera lamapiri la Efuraimu+ mpaka kukadutsanso m’dera la Salisa,+ koma abuluwo sanawapeze. Atatero anadutsa m’dera la Saalimu, ndipo sanawapezenso kumeneko. Kenako anadutsa m’dera la Abenjamini, koma kumenekonso sanawapeze.