10 Kum’mwera kwa malirewo linali gawo la Efuraimu, ndipo kumpoto linali gawo la Manase lomwe linakathera kunyanja.+ Kumpoto, derali linakakumana ndi gawo la Aseri, ndipo kum’mawa linakakumana ndi gawo la Isakara.
16 Kenako ana a Yosefe anati: “Dera lamapiri silitikwanira, ndiponso Akanani a kuchigwa, a ku Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira, ndiponso a kuchigwa cha Yezereeli,+ ali ndi magaleta ankhondo+ okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo.”