38 Kuchokera m’fuko la Gadi,+ anawapatsa mzinda wothawirako munthu amene wapha mnzake, wa Ramoti ku Giliyadi,+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Anawapatsanso Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto,
3 Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inauza atumiki ake kuti: “Kodi mukudziwa kuti mzinda wa Ramoti-giliyadi+ ndi wathu? Koma tikuzengereza kuulanda m’manja mwa mfumu ya Siriya.”