2 Koma Yehoseba+ mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pakati pa ana aamuna a mfumu amene anayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi pamodzi ndi mlezi wake n’kukamubisa+ m’chipinda chamkati chogona kuti Ataliya asamuone, moti sanaphedwe.