25 pazipata za mzindawu padzalowa mafumu ndi akalonga+ okhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mafumuwo pamodzi ndi akalonga awo adzalowa atakwera magaleta ndi mahatchi. Adzalowa pamodzi ndi anthu a mu Yuda komanso anthu okhala mu Yerusalemu ndipo mumzindawu mudzakhala anthu mpaka kalekale.
4 Mukatsatiradi mawu amenewa, pazipata za nyumba iyi padzalowa mafumu okhala pampando wachifumu wa Davide.+ Mfumu iliyonse idzalowa pamodzi ndi atumiki ake ndi anthu ake atakwera magaleta ndi mahatchi.”’+