27 Pomalizira pake, mfumu ya Mowabu inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa amene akanalowa ufumu m’malo mwake, n’kumupereka+ nsembe yopsereza pakhoma. Choncho panabuka mkwiyo waukulu kwambiri wokwiyira Aisiraeli, motero iwo analeka kumenyana ndi mfumu ya Mowabu ndipo anabwerera kwawo.