22 Komabe, popeza ndinalandira thandizo+ kuchokera kwa Mulungu, ndikupitiriza kuchitira umboni kwa anthu otchuka ndi kwa anthu wamba mpaka lero. Sindikunena kena kalikonse koma zokhazo zimene Zolemba za aneneri+ ndi za Mose+ zinaneneratu kuti zidzachitika.