Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pakuti kwa ife kwabadwa mwana.+ Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,+ ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wosatha,+ Kalonga Wamtendere.+

  • Yeremiya 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+

  • Yeremiya 33:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 M’masiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo ndidzameretsera Davide mphukira yolungama+ ndipo mphukirayo idzaweruza mwachilungamo m’dzikoli.+

  • Ezekieli 34:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndidzazipatsa m’busa mmodzi,+ amene ndi mtumiki wanga Davide,+ ndipo adzazidyetsa. Iye adzakhala m’busa wawo ndipo adzazidyetsadi.+

  • Mika 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Iwe Betelehemu Efurata,+ ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda.+ Komabe mwa iwe+ mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli,+ amene adzachite chifuniro changa. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.+

  • Malaki 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Taonani! Ine nditumiza mthenga wanga+ ndipo iye adzandikonzera njira.+ Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi+ Wake.+ Adzabwera ndi mthenga+ wa pangano+ amene mukumuyembekezera mosangalala.+ Iye adzabwera ndithu,” watero Yehova wa makamu.+

  • Luka 24:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Pamenepo anayamba kuwatanthauzira zinthu zokhudza iyeyo m’Malemba onse, kuyambira ndi Zolemba za Mose+ ndi za aneneri zonse.+

  • Luka 24:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Ndiyeno anawauza kuti: “Pamene ndinali nanu limodzi+ ndinakuuzani mawu akuti, zonse zokhudza ine zolembedwa m’chilamulo cha Mose, m’Zolemba za aneneri+ ndi m’Masalimo+ ziyenera kukwaniritsidwa.”

  • Aroma 3:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Koma tsopano, zaonekera kuti munthu akhoza kukhala wolungama kwa Mulungu+ popanda kutsatira Chilamulo. Zimenezi zinatchulidwanso+ m’Chilamulo+ ndi m’Zolemba za aneneri.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena