Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 7:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Choncho Yehovayo akupatsani chizindikiro anthu inu: Tamverani! Mtsikana+ adzatenga pakati+ ndipo adzabereka mwana wamwamuna.+ Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli.

  • Yesaya 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pakuti kwa ife kwabadwa mwana.+ Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,+ ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wosatha,+ Kalonga Wamtendere.+

  • Yeremiya 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+

  • Ezekieli 34:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Ndidzazipatsa m’busa mmodzi,+ amene ndi mtumiki wanga Davide,+ ndipo adzazidyetsa. Iye adzakhala m’busa wawo ndipo adzazidyetsadi.+

  • Danieli 9:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 “Pali milungu 70 imene yaikidwa yokhudza anthu a mtundu wako+ ndi mzinda wanu woyera,+ ndi cholinga choti athetse kuphwanya malamulo,+ athetse machimo,+ aphimbe cholakwa,+ abweretse chilungamo kuti chikhalepo mpaka kalekale,+ adinde chidindo+ pa masomphenya ndi maulosi, ndiponso kuti adzoze Malo Opatulikitsa.+

  • Mika 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Iwe Betelehemu Efurata,+ ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda.+ Komabe mwa iwe+ mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli,+ amene adzachite chifuniro changa. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.+

  • Malaki 3:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Taonani! Ine nditumiza mthenga wanga+ ndipo iye adzandikonzera njira.+ Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi+ Wake.+ Adzabwera ndi mthenga+ wa pangano+ amene mukumuyembekezera mosangalala.+ Iye adzabwera ndithu,” watero Yehova wa makamu.+

  • Yohane 1:45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Kenako Filipo anapeza Natanayeli+ n’kumuuza kuti: “Uja amene Mose analemba za iye m’Chilamulo+ komanso wotchulidwa m’Zolemba za aneneri,+ ife tam’peza. Iyeyu ndi Yesu, mwana wa Yosefe,+ wa ku Nazareti.”

  • Machitidwe 10:43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Aneneri onse amachitira umboni za iyeyu,+ kuti aliyense womukhulupirira, machimo ake amakhululukidwa m’dzina lake.”+

  • Machitidwe 26:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Komabe, popeza ndinalandira thandizo+ kuchokera kwa Mulungu, ndikupitiriza kuchitira umboni kwa anthu otchuka ndi kwa anthu wamba mpaka lero. Sindikunena kena kalikonse koma zokhazo zimene Zolemba za aneneri+ ndi za Mose+ zinaneneratu kuti zidzachitika.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena