-
Danieli 9:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 “Pali milungu 70 imene yaikidwa yokhudza anthu a mtundu wako+ ndi mzinda wanu woyera,+ ndi cholinga choti athetse kuphwanya malamulo,+ athetse machimo,+ aphimbe cholakwa,+ abweretse chilungamo kuti chikhalepo mpaka kalekale,+ adinde chidindo+ pa masomphenya ndi maulosi, ndiponso kuti adzoze Malo Opatulikitsa.+
-
-
Chivumbulutso 19:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Pamenepo ndinagwada pansi n’kuwerama patsogolo pa mapazi ake kuti ndimulambire.+ Koma iye anandiuza kuti:+ “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.+ Lambira Mulungu,+ pakuti kuchitira umboni za Yesu ndiko cholinga cha maulosi.”+
-