Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Mbiri 17:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “‘“Masiku ako akadzakwana kuti ukakhale pamodzi ndi makolo ako,+ pamenepo ndithu ndidzautsa mbewu yako yobwera pambuyo pako,+ imene idzakhala mmodzi wa ana ako, ndipo ndidzakhazikitsadi ufumu wake.+

  • Yesaya 4:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 M’tsiku limenelo, chinthu chimene Yehova adzachiphukitse+ chidzakhala chokongoletsera ndi chaulemerero.+ Zipatso za m’dzikolo zidzakhala zonyaditsa+ ndi zokongola kwa Aisiraeli amene adzapulumuke.+

  • Yesaya 11:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nthambi+ idzatuluka pachitsa cha Jese,+ ndipo mphukira+ yotuluka pamizu yake idzakhala yobereka zipatso.+

  • Yesaya 53:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pa winawake, ndiponso ngati muzu m’dziko lopanda madzi. Alibe maonekedwe alionse apamwamba kapena okongola,+ ndipo maonekedwe ake si osiririka m’maso mwathu.+

  • Yeremiya 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “ndipo Davide ndidzamuutsira mphukira yolungama.+ Ndithudi mfumu idzalamulira+ m’dzikoli ndi kuchita zinthu mozindikira, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+

  • Zekariya 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “‘Tamvera iwe Yoswa mkulu wa ansembe ndi anzako amene akhala pansi pamaso pako, pakuti iwo ndi amuna amene ali ngati zizindikiro zolosera zam’tsogolo.+ Ine ndibweretsa mtumiki wanga+ dzina lake Mphukira.+

  • Zekariya 6:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ndiyeno udzamuuze kuti,

      “‘Yehova wa makamu wanena kuti: “Munthu uyu+ dzina lake ndi Mphukira.+ Adzaphuka pamalo ake ndipo adzamanga kachisi wa Yehova.+

  • Chivumbulutso 22:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 “‘Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kudzachitira umboni zinthu izi kwa inu, kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu+ ndi mbadwa+ ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena