20 Ndiyeno ku chiyambi kwa chaka,+ pa nthawi imene mafumu anali kupita kukamenya nkhondo,+ Yowabu anatsogolera gulu lankhondo+ n’kukawononga dziko la ana a Amoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba.+ Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu. Tsopano Yowabu uja anapha anthu+ ku Raba n’kuwononga mzindawo.