20 Panabukanso nkhondo ina ku Gati,+ pa nthawi imene kunali munthu wa msinkhu waukulu modabwitsa. Iye anali ndi zala 6 kudzanja lililonse ndiponso zala 6 kuphazi lililonse, moti anali ndi zala 24 zonse pamodzi. Ameneyunso anali mmodzi mwa mbadwa za Arefai.+