12 Mfumuyo inapanga zochirikizira nyumba ya Yehova+ ndi nyumba ya mfumu, pogwiritsira ntchito matabwa a m’bawawo. Inapanganso azeze+ ndi zoimbira za zingwe+ n’kupatsa oimba. Matabwa a m’bawa ochuluka chonchi sanayambe abwerapo kapena kuonedwapo mpaka lero.