33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukupitikitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja,+ ndipo mizinda yanu idzawonongedwa ndi kukhala mabwinja.
9 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+