12 Idzaika anthu ena kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000+ ndi atsogoleri a magulu a anthu 50.+ Ena azidzalima minda yake+ ndi kukolola mbewu zake,+ ndiponso ena azidzapanga zida zake zankhondo+ ndi zida zogwiritsa ntchito pamagaleta ake.+
7 Iye anauza atumiki ake amene anali atamuzungulirawo kuti: “Tamverani inu Abenjamini. Kodi nayenso mwana wa Jese+ adzakupatsani minda ya mpesa ndi minda ya mbewu zina?+ Kodi nonsenu adzakuikani kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000+ ndi atsogoleri a magulu a anthu 100?