Deuteronomo 23:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Pakuti Yehova Mulungu wanu akuyendayenda mumsasa wanu kuti akulanditseni+ ndi kupereka adani anu m’manja mwanu.+ Choncho msasa wanu uzikhala woyera,+ kuti asaone choipa chilichonse pakati panu ndi kutembenuka n’kuleka kuyenda nanu limodzi.+ Oweruza 4:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Kenako Debora anauza Baraki kuti: “Nyamuka, pakuti lero ndi tsiku limene Yehova adzapereka Sisera m’manja mwako. Yehova akuyendatu patsogolo pako.”+ Ndipo Baraki anatsikadi m’phiri la Tabori, amuna 10,000 akum’tsatira. Yesaya 45:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Ine ndidzakhala kutsogolo kwako+ ndipo ndidzasalaza zitunda za m’dzikolo.+ Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zamkuwa ndipo ndidzadula mipiringidzo yachitsulo.+
14 Pakuti Yehova Mulungu wanu akuyendayenda mumsasa wanu kuti akulanditseni+ ndi kupereka adani anu m’manja mwanu.+ Choncho msasa wanu uzikhala woyera,+ kuti asaone choipa chilichonse pakati panu ndi kutembenuka n’kuleka kuyenda nanu limodzi.+
14 Kenako Debora anauza Baraki kuti: “Nyamuka, pakuti lero ndi tsiku limene Yehova adzapereka Sisera m’manja mwako. Yehova akuyendatu patsogolo pako.”+ Ndipo Baraki anatsikadi m’phiri la Tabori, amuna 10,000 akum’tsatira.
2 “Ine ndidzakhala kutsogolo kwako+ ndipo ndidzasalaza zitunda za m’dzikolo.+ Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zamkuwa ndipo ndidzadula mipiringidzo yachitsulo.+