Numeri 10:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ana a Aroni, ansembewo, ndiwo aziliza malipengawo.+ Ndi lamulo kwa inu kugwiritsa ntchito malipengawa m’mibadwo yanu yonse mpaka kalekale.* 1 Mbiri 15:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Sebaniya, Yosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya, ndi Eliezere, anali ansembe omwe anali kuimba malipenga mokweza+ patsogolo pa likasa la Mulungu woona. Obedi-edomu ndi Yehiya anali alonda a Likasa. 2 Mbiri 29:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Choncho Aleviwo anaimirirabe atanyamula zipangizo zoimbira+ za Davide. Iwo anaimirira pamodzi ndi ansembe omwe ananyamula malipenga.+
8 Ana a Aroni, ansembewo, ndiwo aziliza malipengawo.+ Ndi lamulo kwa inu kugwiritsa ntchito malipengawa m’mibadwo yanu yonse mpaka kalekale.*
24 Sebaniya, Yosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya, ndi Eliezere, anali ansembe omwe anali kuimba malipenga mokweza+ patsogolo pa likasa la Mulungu woona. Obedi-edomu ndi Yehiya anali alonda a Likasa.
26 Choncho Aleviwo anaimirirabe atanyamula zipangizo zoimbira+ za Davide. Iwo anaimirira pamodzi ndi ansembe omwe ananyamula malipenga.+