33 Nsalu yotchingayi uipachike m’munsi mwa ngowe zolumikizira nsalu zapamwamba pa chihema, ndipo uike likasa la umboni+ kuseri kwa nsalu yotchingayi. Nsaluyi ikhale malire pakati pa Malo Oyera+ ndi Malo Oyera Koposa.+
6 Kenako ansembe anabweretsa likasa+ la pangano la Yehova kumalo ake,+ kuchipinda chamkati cha nyumbayo, Malo Oyera Koposa, ndipo analiika pansi pa mapiko a akerubi.+
24 Pakuti Khristu sanalowe m’malo oyera amkatikati opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Tsopano ali kumwamba kuti aonekere pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.+