29 Choncho mfumu Yehoramu+ inabwerera n’kupita ku Yezereeli+ kuti ikachire zilonda zimene Asiriya anaivulaza ku Rama, pamene inali kumenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya. Chotero Ahaziya+ mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anali kudwala.