6 Choncho Yehoramu anabwerera n’kupita ku Yezereeli+ kuti akachire zilonda zimene anam’vulaza ku Rama,+ pamene anali kumenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.
Chotero Azariya+ mwana wa Yehoramu+ mfumu ya Yuda anapita ku Yezereeli kukaona Yehoramu+ mwana wa Ahabu chifukwa anali kudwala.+