-
2 Samueli 4:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Yonatani+ mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna wolumala mapazi.+ Mwanayu anali ndi zaka zisanu pamene kunabwera uthenga wa imfa ya Sauli ndi Yonatani kuchokera ku Yezereeli.+ Uthengawu utafika, mlezi wake anamunyamula ndi kuthawa naye. Pamene anali kuthawa mwamantha, mleziyo anagwetsa mwanayo ndipo analumala. Mwanayo dzina lake anali Mefiboseti.+
-