16 Kenako ana a Yosefe anati: “Dera lamapiri silitikwanira, ndiponso Akanani a kuchigwa, a ku Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira, ndiponso a kuchigwa cha Yezereeli,+ ali ndi magaleta ankhondo+ okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo.”
33 Ndiyeno Amidiyani+ ndi Aamaleki onse,+ pamodzi ndi anthu onse a Kum’mawa+ anasonkhana pamodzi+ ndi kuwoloka mtsinje, ndipo anamanga msasa wawo m’chigwa cha Yezereeli.+