9 “Ndiyeno upange bwalo+ la chihema chopatulika. Kumbali ya ku Negebu, chakum’mwera, bwalolo ulitchinge ndi mpanda wa nsalu za ulusi wopota wabwino kwambiri.+ Mpandawo ukhale mikono 100 m’litali mwake kumbali imodziyo.
16 Aroni ndi ana ake azidya zotsala za nsembe imeneyi.+ Azipanga mkate wopanda chofufumitsa+ ndi kudya mkatewo m’malo oyera. Aziudyera m’bwalo la chihema chokumanako.