2 Pomalizira pake mfumu ya Asuri inatuma Rabisake+ kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu.+ Inamutumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali amphamvu. Iye anakaima pangalande+ yochokera kudziwe lakumtunda,+ pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+