27“Upange guwa lansembe la matabwa a mthethe, m’litali mikono isanu, ndipo m’lifupi mikono isanu. Guwalo+ likhale lofanana muyezo wake mbali zake zonse zinayi, ndipo msinkhu wake likhale mikono itatu.
48 M’kupita kwa nthawi, Solomo anapanga ziwiya zonse za panyumba ya Yehova, za paguwa lansembe+ lagolide, ndi za patebulo+ limene ankaikapo mkate wachionetsero.