15 Tsopano mtengowo wafika poti munthu akhoza kuusandutsa nkhuni. Chotero iye watenga mbali ya mtengowo kuti asonkhere moto woti aziwotha. Wayatsa motowo n’kuphikapo mkate. Wasemanso mulungu woti azimugwadira.+ Mtengowo waupanga chifaniziro chosema+ ndipo akuchigwadira n’kumachilambira.