5 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+
9 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo,* chifukwa cha zolakwa za anthu odana ndi ine.+
14 Koma pobwerera kuchokera kokapha Aedomu, Amaziya anatenga milungu+ ya ana a Seiri n’kukaiimika kuti ikhale milungu yake.+ Kenako anayamba kuigwadira+ ndi kuifukizira nsembe yautsi.+
20 Koma anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi, sanalape ntchito za manja awo.+ Sanalape kulambira ziwanda+ ndi mafano agolide, asiliva,+ amkuwa, amwala, ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva, kapena kuyenda.+