Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 26:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 “‘Musadzipangire milungu yopanda pake,+ chifaniziro,+ kapena chipilala chopatulika. Musaike mwala wokhala ndi zithunzi zojambula mochita kugoba+ m’dziko lanu kuti muziugwadira,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.

  • Oweruza 17:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndiyeno anabweza ndalama zasiliva zokwana 1,100 zija kwa mayi ake.+ Atabweza ndalamazo, mayi akewo anati: “Ndithudi ndipereka ndalama zasilivazi kwa Yehova kuti zikhale zopatulika. Ndichita zimenezi kuti ndithandize mwana wanga, ndi kuti papangidwe chifaniziro chosema+ ndiponso chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Tsopano ndikubweza ndalamazi kwa iwe.”

  • Oweruza 18:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Kenako ana a Dani anadziimikira chifaniziro chosema+ chija, ndipo Yonatani+ mwana wa Gerisomu,+ mwana wa Mose, pamodzi ndi ana ake, anakhala ansembe a fuko la Dani kufikira tsiku limene anthu a m’dzikolo anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.+

  • 2 Mafumu 21:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Komanso iye anaika m’nyumbayo chifaniziro+ cha mzati wopatulika chimene anapanga. Koma ponena za nyumba imeneyo,+ Yehova anauza Davide ndi Solomo mwana wake kuti: “M’nyumba iyi ndiponso mu Yerusalemu mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Isiraeli, ndidzaikamo dzina langa mpaka kalekale.+

  • Nahumu 1:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Koma ponena za iwe, Yehova walamula kuti, ‘Sudzakhalanso ndi ana otchedwa ndi dzina lako.+ Ndidzadula zifaniziro zosema ndi zifaniziro zopangidwa ndi chitsulo chosungunula+ ndipo ndidzazitaya kunja kwa nyumba za milungu yako. Ndidzakukonzera manda+ chifukwa ndiwe wopanda pake.’

  • Habakuku 2:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kodi chifaniziro chosema, chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndiponso mphunzitsi wonama,+ zili ndi phindu lanji+ kuti wozipanga azizikhulupirira+ ndipo azipanga milungu yopanda pake yosalankhula?+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena