3 moti akupita kukalambira milungu ina ndi kuigwadira, kapena kugwadira dzuwa, mwezi kapena khamu lonse la zinthu zakuthambo,+ chinthu chimene ine sindinakulamuleni,+
15 “‘Wotembereredwa ndi munthu aliyense wopanga chifaniziro chosema+ kapena chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula+ ndi kuchibisa. Chifanizirocho ndi chinthu chonyansa kwa Yehova,+ Mulungu wopanga manja a mmisiri wa matabwa ndi zitsulo.’+ (Anthu onse ayankhe kuti, ‘Zikhale momwemo!’)*+
18 Amuna asanuwo analowa m’nyumba ya Mika ndi kutenga chifaniziro chosema, efodi, aterafi ndi chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ Atatero wansembeyo+ anawafunsa kuti: “Mukutani kodi?”