25 Choncho ophunzira enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anati: “Ndithu ndikapanda kuona mabala a misomali m’manja mwawo ndi kuika chala changa m’mabala a misomaliwo, ndiponso kuika dzanja langa m’mbali mwa mimba yawo,+ ine sindikhulupirira ayi.”+