-
Nehemiya 1:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Aa, Yehova. Chonde, tcherani khutu ku pemphero la ine mtumiki wanu ndiponso pemphero+ la atumiki anu amene amasangalala ndi kuopa dzina lanu.+ Chonde, ndithandizeni ine mtumiki wanu kuti zinthu zindiyendere bwino lero+ ndipo mwamunayu andimvere chisoni.”+
Pa nthawi imeneyi, ine ndinali woperekera chikho+ kwa mfumu.
-
-
Nehemiya 2:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Komanso andipatse kalata yopita kwa Asafu amene akuyang’anira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokamangira zipata za Nyumba ya Chitetezo Champhamvu+ ya kukachisi,+ mpanda+ wa mzindawo ndiponso nyumba imene ndizikakhalamo.” Choncho mfumu inandipatsa makalatawo, chifukwa Mulungu anandikomera mtima.+
-