29Tsopano mfumu Davide inauza mpingo wonse+ kuti: “Solomo mwana wanga, amene Mulungu wamusankha,+ ndi wamng’ono+ ndi wosakhwima. Koma ntchitoyi ndi yaikulu chifukwa chinyumba chachikuluchi, si cha munthu ayi,+ koma ndi cha Yehova Mulungu.
3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye.+ Choncho apite ku Yerusalemu m’dziko la Yuda n’kukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, yomwe inali ku Yerusalemu.+ Iye ndiye Mulungu woona.+