6 Tsopano Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova.+ Anayamba kuchita zimenezi m’chaka cha 480 kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo,+ m’mwezi wachiwiri+ wa Zivi.+ Ichi chinali chaka chachinayi+ cha ulamuliro wake monga mfumu ya Isiraeli.