17 “Tsopano ngati inu mfumu mukuona kuti n’koyenera, uzani anthu afufuze+ m’nyumba ya chuma cha mfumu imene ili ku Babuloko, kuti aone ngati mfumu Koresi inaikadi lamulo+ loti nyumba ya Mulungu yomwe ili ku Yerusalemu imangidwenso. Inu mfumu mutitumizire chigamulo chanu pankhani imeneyi.”