22 Kwa masiku 7, iwo anachita mosangalala chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ pakuti Yehova anawachititsa kusangalala. Iye anatembenuzira+ kwa iwo mtima wa mfumu ya Asuri kuti ilimbitse manja awo pa ntchito yomanga nyumba ya Mulungu woona, Mulungu wa Isiraeli.