-
Ezara 9:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Ngakhale kuti ndife akapolo,+ Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathuwo,+ koma watisonyeza kukoma mtima kosatha pamaso pa mafumu a ku Perisiya.+ Wachita zimenezi kuti atitsitsimutse n’cholinga choti tikamange nyumba ya Mulungu wathu+ komanso tikakonze malo ozungulira nyumbayo amene anali bwinja,+ ndi kuti tikhale mu Yuda ndi mu Yerusalemu ngati kuti tili mumpanda wamiyala.+
-
-
Nehemiya 1:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Aa, Yehova. Chonde, tcherani khutu ku pemphero la ine mtumiki wanu ndiponso pemphero+ la atumiki anu amene amasangalala ndi kuopa dzina lanu.+ Chonde, ndithandizeni ine mtumiki wanu kuti zinthu zindiyendere bwino lero+ ndipo mwamunayu andimvere chisoni.”+
Pa nthawi imeneyi, ine ndinali woperekera chikho+ kwa mfumu.
-