16 Ndipo ndidziwa bwanji kuti mwandikomera mtima, ineyo ndi anthu anu? Si mwa kuyenda nafe kodi?+ Pajatu ine ndi anthu anu mwatisiyanitsa ndi anthu ena onse amene ali padziko lapansi.”+
21 Ndiyeno ana a Isiraeli amene anabwera kuchokera ku ukapolo anadya+ nyamayo. Komanso aliyense amene anadzilekanitsa ku zonyansa+ za anthu a mitundu ina ya m’dzikolo n’kubwera kwa iwo ndi kufunafuna Yehova Mulungu wa Isiraeli, anadya nawo.+
2 Pamenepo mbewu ya Isiraeli inadzipatula+ kwa anthu onse osakhala Aisiraeli.+ Atatero anaimirira ndi kuulula+ machimo awo+ ndi zolakwa za makolo awo.+