24 Atsogoleri a Alevi anali Hasabiya, Serebiya+ ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyeli.+ Ndipo abale awo anaima moyang’anizana nawo kuti azitamanda ndi kuyamika Mulungu mogwirizana ndi lamulo+ la Davide, munthu wa Mulungu woona. Gulu lililonse la alonda linaima moyandikana ndi gulu lina la alonda.