Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 12:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ndiyeno Yehova anaonekera kwa Abulamu n’kumuuza kuti: “Ndidzapereka dziko ili+ kwa mbewu yako.”+ Pambuyo pake, iye anamanga pamalopo guwa lansembe la Yehova, yemwe anaonekera kwa iye.

  • Genesis 15:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu,+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+

  • Genesis 17:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Dziko limene ukukhalamo ngati mlendoli,+ ndidzalipereka kwa iwe ndi mbewu yako yobwera pambuyo pako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala lawo mpaka kalekale, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”+

  • Genesis 26:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ukhale ngati mlendo m’dzikoli,+ ndipo ndidzapitiriza kukhala nawe ndi kukudalitsa, chifukwa mayiko onsewa ndidzawapereka kwa iwe ndi kwa mbewu yako.+ Ndidzakwaniritsa lumbiro limene ndinalumbirira Abulahamu bambo ako.+

  • Deuteronomo 9:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Sikuti mukulowa m’dziko ili kukalitenga kukhala lanu chifukwa cha kulungama kwanu+ kapena chifukwa cha kuwongoka mtima kwanu.+ Yehova Mulungu wanu akukankhira mitundu iyi kutali ndi inu, kwenikweni chifukwa cha kuipa kwawo,+ ndiponso kuti Yehova akwaniritse mawu onse amene analumbirira makolo anu Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena