-
Nehemiya 13:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndiyeno ndinaika Selemiya wansembe, Zadoki wokopera Malemba ndi Pedaya mmodzi mwa Alevi, kuti akhale oyang’anira malo osungira zinthu. Amenewa anali kuyang’anira Hanani mwana wa Zakuri amene anali mwana wa Mataniya,+ pakuti anthu anali kuwaona kuti ndi okhulupirika.+ Iwowa anapatsidwa udindo wogawa+ zinthu kwa abale awo.
-