9 pali mmodzi yekha amene ali njiwa yanga,+ wopanda chilema.+ Iye ndiye mwana wamkazi wapadera kwambiri kwa mayi ake. Iyeyo ndi wosadetsedwa kwa mayi amene anam’bereka. Ana aakazi atamuona, anamutcha wodala. Mafumukazi ndi adzakazi anamutamanda+ kuti,