14 Pamenepo anthuwo anafuulira Yehova ndi kunena kuti:+ “Chonde inu Yehova, musalole kuti tiwonongeke chifukwa cha munthu uyu! Musaike pa ife mlandu wa magazi a munthu wosalakwa,+ chifukwa zonsezi zachitika pokwaniritsa chifuniro chanu, inu Yehova!”+